Jeremiah 36:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
adapita ku nyumba ya mfumu, nakaloŵa m'chipinda cha mlembi. Akuluakulu onse anali atasonkhana m'menemo: mlembi Elisama, Delaya mwana wa Semaya, Elinatani mwana wa Akobori, Gemariya mwana wa Safani, Zedekiya mwana wa Hananiya, pamodzi ndi akuluakulu ena onse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
anatsikira kunyumba ya mfumu, nalowa m'chipinda cha mlembi; ndipo, taonani, akulu onse analikukhalamo, Elisama mlembi, ndi Delaya mwana wa Semaya, ndi Elinatani mwana wa Akibori, ndi Gemariya mwana wa Safani, ndi Zedekiya mwana wa Hananiya, ndi akulu onse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
anapita ku nyumba ya mfumu nakalowa ku chipinda cha mlembi. Akuluakulu, mlembi Elisama, Delaya mwana wa Semaya, Elinatani mwana wa Akibori, Gemariya mwana wa Safani, Zedekiya mwana wa Hananiya pamodzi ndi akuluakulu ena onse, anali atasonkhana kumeneko.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
anatsikira ku nyumba ya mfumu, nalowa m'cipinda ca mlembi; ndipo, taonani, akuru onse analikukhalamo, Elisama mlembi, ndi Delaya mwana wa Semaya, ndi Elinatani mwana wa Akibori, ndi Gemariya mwana wa Safani, ndi Zedekiya mwana wa Hananiya, ndi akuru onse.