Jeremiah 36:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamenepo akuluakulu adatuma Yehudi mwana wa Netaniya, mwana wa Selemiya, mwana wa Kusi, kwa Baruki kukamuuza kuti abwere nalo buku limene ankaŵerengera anthu. Motero Baruki mwana wa Neriya, adapita nalo bukulo kwa iwo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake akulu onse anatuma Yehudi mwana wa Netaniya, mwana wa Selemiya, mwana wa Kusi, kwa Baruki, kukanena, Tenga m'dzanja lako mpukutu wauwerenga m'makutu a anthu, nudze kuno. Ndipo Baruki mwana wa Neriya anatenga mpukutuwo m'dzanja lake, nadza kwa iwo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pambuyo pake akuluakulu onsewo anatuma Yehudi mwana wa Netaniya, mwana wa Selemiya, mwana wa Kusi, kwa Baruki kukamuwuza kuti, “Bwera ndi buku limene unawerenga kwa anthu.” Ndipo Baruki mwana wa Neriya anapita nalo bukulo kwa anthuwo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace akuru onse anatuma Yehudi mwana wa Nataniya, mwana wa Salamiya, mwana wa Kusa, kwa Baruki, kukanena, Tenga m'dzanja lako mpukutu wauwerenga m'makutu a anthu, nudze kuno. Ndipo Baruki mwana wa Neriya anatenga mpukutuwo m'dzanja lace, nadza kwa iwo.