Jeremiah 36:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Atamva zimene adaaŵerengazo, adayamba kuyang'anitsitsana ali njenjenje ndi mantha. Tsono adauza Baruki kuti, “Tiyenera kuŵauza amfumu mau onseŵa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo panali, pamene anamva mau onse, anaopa nayang'anana wina ndi mnzake, nati kwa Baruki, Tidzamfotokozeratu mfumu mau awa onse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Atamva mawu onsewo, anayangʼanana mwa mantha ndipo anamuwuza Baruki kuti, “Ndithudi tikafotokozera mfumu mawu onsewa.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo panali, pamene anamva mau onse, anaopa nayang'anana wina ndi mnzace, nati kwa Baruki, Tidzamfotokozeratu mfumu mau awa onse.