Jeremiah 36:23 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yehudi ankati akaŵerenga masamba atatu kapena anai a bukulo, mfumu inkaŵagwira nkuŵadula ndi mpeni, niŵaponya m'malaŵi a moto. Idapitirira kuchita zimenezi mpaka buku lonse lidapsa ndi moto.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo panali, pamene Yehudi anawerenga masamba atatu pena anai, mfumu inawadula ndi kampeni ka mlembi, niwaponya m'moto wa m'mbaulamo, mpaka mpukutu wonse unatha kupsa ndi moto wa m'mbaulamo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehudi ankati akawerenga masamba atatu kapena anayi a bukulo, mfumu inkawangʼamba ndi mpeni ndi kuwaponya pa moto ndipo anapitiriza kuchita zimenezi mpaka buku lonse linapsa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo panali, pamene Yehudi anawerenga masamba atatu pena anai, mfumu inawadula ndi kampeni ka mlembi, niwaponya m'moto wa m'nkhumbaliromo, mpaka mpukutu wonse unatha kupsa ndi moto wa m'nkhumbaliromo.