Jeremiah 36:26 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kenaka mfumu idalamula Yerahamele mwana wa mfumu, Seraya mwana wa Aziriele ndi Selemiya mwana wa Abideele kuti akagwire mlembi Baruki ndi mneneri Yeremiya. Koma Chauta anali ataŵabisa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mfumu inauza Yerameele mwana wake wa mfumu, ndi Seraya mwana wa Aziriele, ndi Selemiya mwana wa Abideele, kuti awagwire Baruki mlembi ndi Yeremiya mneneri; koma Yehova anawabisa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mʼmalo mwake, mfumu inalamula Yerahimeeli mwana wake, Seraya mwana wa Azirieli ndi Selemiya mwana wa Abideeli kuti agwire mlembi Baruki ndi mneneri Yeremiya. Koma pamenepo nʼkuti Yehova atawabisa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mfumu inauza Yeremeeli mwana wace wa mfumu, ndi Seraya mwana wa Azirieli, ndi Selemiya mwana wa Abidieli, kuti awagwire Baruki mlembi ndi Yeremiya mneneri; koma Yehova anawabisa.