Jeremiah 36:29 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo za Yehoyakimu, mfumu ya ku Yuda, ukamuuze kuti, ‘Chauta akuti, Paja iwe udatentha buku lija, nkumanena kuti, “Chifukwa chiyani walemba kuti mfumu ya ku Babiloni idzafika kudzaononga dziko lino ndi kuwononga anthu ndi nyama zomwe?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo za Yehoyakimu mfumu ya Yuda uziti, Yehova atero: Iwe watentha mpukutu uwu, ndi kuti, Bwanji walemba m'menemo, kuti, Mfumu ya ku Babiloni idzadzadi nidzaononga dziko ili, nidzatha m'menemo anthu ndi nyama?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndiponso akamuwuze Yehoyakimu mfumu ya Yuda kuti, ‘Yehova akuti: Iwe unatentha buku lija ndipo unati: Nʼchifukwa chiyani unalemba kuti mfumu ya ku Babuloni idzabwera ndithu kudzawononga dziko lino ndi kupha anthu pamodzi ndi nyama zomwe?’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo za Yehoyakimu mfumu ya Yuda uziti, Yehova atero: Iwe watentha mpukutu uwu, ndi kuti, Bwanji walemba m'menemo, kuti, Mfumu ya ku Babulo idzadzadi nidzaononga dziko ili, nidzatha m'menemo anthu ndi nvama?