Jeremiah 36:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mwina mwake banja la Yuda lidzamva za zoopsa zonse zimene ndikuti ndiŵagwetsere. Choncho munthu aliyense adzasiya makhalidwe ake oipa. Motero ndidzaŵakhululukira zolakwa zao ndi machimo ao.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kapena nyumba ya Yuda idzamva choipa chonse chimene nditi ndidzawachitire; kuti abwerere yense kuleka njira yake yoipa; kuti ndikhululukire mphulupulu yao ndi tchimo lao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mwina mwake anthu a ku Yuda adzamva za zoopsa zonse zimene ndakonza kuti ndiwachitire, ndipo munthu aliyense adzatembenuka ndi kusiya ntchito zake zoyipa. Motero ndidzawakhululukira zoyipa zawo ndi machimo awo.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kapena nyumba ya Yuda idzamva coipa conse cimene nditi ndidzawacitire; kuti abwerere yense kuleka njira yace yoipa; kuti ndikhululukire mphulupulu yao ndi cimo lao.