Jeremiah 36:30 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nchifukwa chake za Yehoyakimu, mfumu ya ku Yuda, Chauta akunena kuti sipadzaoneka wina woloŵa m'malo mwake pa mpando waufumu wa Davide. Akadzafa, mtembo wake masana udzakhala pa dzuŵa, ndipo usiku udzakhala pa chisanu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake Yehova atero za Yehoyakimu mfumu ya Yuda: Adzasowa wokhala pa mpando wachifumu wa Davide; ndipo mtembo wake udzaponyedwa usana kunja kuli dzuwa, ndi usiku kuli chisanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nʼchifukwa chake kunena za Yehoyakimu mfumu ya Yuda Yehova akuti sipadzaoneka munthu wina wolowa mʼmalo mwake pa mpando wa Davide. Akadzafa mtembo wake udzaponyedwa kunja ndipo udzakhala pa dzuwa masana, ndi pachisanu chowundana usiku.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace Yehova atero za Yehoyakimu mfumu ya Yuda: Adzasowa wokhala pa mpando wacifumu wa Davide; ndipo mtembo wace udzaponyedwa usana kunja kuli dzuwa, ndi usiku kuli cisanu.