Jeremiah 36:31 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidzamlanga pamodzi ndi zidzukulu zake ndi aphungu ake chifukwa cha zoipa zao. Ndidzaŵagwetsera iwowo ndi anthu onse a ku Yerusalemu ndi a ku Yuda zoopsa zonse zimene ndidanena, chifukwa iwo sadamvere mau anga.’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndidzamlanga iye ndi mbeu zake ndi atumiki ake chifukwa cha mphulupulu zao; ndipo ndidzawatengera iwo, ndi okhala m'Yerusalemu, ndi anthu a Yuda, zoipa zonse ndawanenera iwo, koma sanamvere.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndidzamulanga pamodzi ndi ana ake ndiponso omutumikira ake chifukwa cha zoyipa zawo; ndidzagwetsa pa iwo ndi pa onse amene akukhala mu Yerusalemu ndiponso pa anthu a ku Yuda masautso onse amene ndinawanena, chifukwa sanamvere.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndidzamlanga iye ndi mbeu zace ndi atumiki ace cifukwa ca mphulupulu zao; ndipo ndidzawatengera iwo, ndi okhala m'Yerusalemu, ndi anthu a Yuda, zoipa zonse ndawanenera iwo, koma sanamvera.