Jeremiah 36:32 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Yeremiya adatenga buku lina napatsa mlembi Baruki, mwana wa Neriya, namlembetsa mau onse a m'buku limene Yehoyakimu mfumu ya ku Yuda adatentha lija. Ndipo adaonjezerapo mau ambiri monga omwewo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yeremiya anatenga mpukutu wina, naupereka kwa Baruki mlembi, mwana wa Neriya; amene analemba m'menemo ponena Yeremiya mau onse a m'buku lija Yehoyakimu mfumu ya Yuda analitentha m'moto; ndipo anaonjezapo mau ambiri oterewa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho Yeremiya anatenga buku lina napatsa mlembi Baruki mwana wa Neriya, ndipo Yeremiya anamulembetsa mawu onse amene anali mʼbuku limene Yehoyakimu mfumu ya Yuda anatentha. Ndipo anawonjezerapo mawu ambiri monga omwewo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika