Jeremiah 36:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndiye tsono upite ndiwe kumeneko m'malo mwanga pa tsiku losala chakudya, ukaŵerenge mau a Chauta amene ndidakulembetsa m'bukumu, anthu onse alikumva. Udzaŵaŵerenge kwa anthu onse a ku Yuda amene abwera kuchokera ku mizinda yao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
koma pita iwe, nuwerenge mu mpukutu umene ndakulembetsa, mau a Yehova m'makutu a anthu m'nyumba ya Yehova tsiku lakusala kudya; ndiponso udzawawerenga m'makutu a Ayuda onse amene atuluka m'midzi yao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono iwe upite ku Nyumba ya Yehova pa tsiku losala kudya ndipo ukawerenge mawu a Yehova ochokera mʼbukumu amene ndinakulembetsa anthu onse akumva. Ukawawerengere anthu onse a ku Yuda amene amabwera ku Nyumba ya Mulungu kuchokera ku mizinda yawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
koma pita iwe, nuwerenge mu mpukutu umene ndakulembetsa, mau a Yehova m'makutu a anthu m'nyumba ya Yehova tsiku lakusala kudya; ndiponso udzawawerenga m'makutu a Ayuda onse amene aturuka m'midzi yao.