Jeremiah 36:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Motero Baruki mwana wa Neriya adachita zonse zimene mneneri Yeremiya adamuuza kuti achite. Adaŵerenga mau a Chauta olembedwa m'buku aja m'Nyumba ya Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Baruki mwana wa Neriya anachita monga mwa zonse anamuuza iye Yeremiya mneneri, nawerenga m'buku mau a Yehova m'nyumba ya Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Baruki mwana wa Neriya anachita zonse zimene mneneri Yeremiya anamuwuza kuti achite. Mʼnyumba ya Yehova, iye anawerenga mawu a Yehova ochokera mʼbukulo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Baruki mwana wa Neriya anacita monga mwa zonse anamuuza iye Yeremiya mneneri, nawerenga m'buku mau a Yehova m'nyumba ya Yehova.