Jeremiah 36:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pa mwezi wachisanu ndi chinai wa chaka chachisanu cha ufumu wa Yehoyakimu mwana wa Yosiya mfumu ya ku Yuda, anthu onse a ku Yerusalemu ndi onse amene adaabwera kumeneko kuchokera ku mizinda ya Yuda, adapangana za kusala chakudya kuti apepese Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo panali chaka chachisanu cha Yehoyakimu mwana wa Yosiya, mfumu ya Yuda, mwezi wachisanu ndi chinai, anthu onse a m'Yerusalemu, ndi anthu onse ochokera m'midzi ya Yuda kudza ku Yerusalemu, analalikira kusala kudya pamaso pa Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pa mwezi wachisanu ndi chinayi wa chaka chachisanu cha Yehoyakimu mwana wa Yosiya mfumu ya Yuda, anthu onse a mu Yerusalemu ndi onse amene anabwera kumeneko kuchokera ku mizinda ya Yuda, anapangana za kusala kudya kuti apepese Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo panali caka cacisanu ca Yehoyakimu mwana wa Yosiya, mfumu ya Yuda, mwezi wacisanu ndi cinai, anthu onse a m'Yerusalemu, ndi anthu onse ocokera m'midziya Yuda kudzaku Yerusalemu, analalikira kusala kudya pamaso pa Yehova.