Jeremiah 37:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ngakhale mutagonjetsa gulu lonse la Ababiloni limene mukumenyana nalo nkhondo, ngakhalenso mwa iwowo mutatsala ovulala okhaokha m'mahema mwao, iwo omwewo adzadzambatuka nkuutentha mzindawu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti ngakhale mukadakantha nkhondo yonse ya Ababiloni akumenyana nanu, ngakhale akadatsala olasidwa okhaokha mwa iwo, koma iwowa akadauka yense m'hema wake ndi kutentha mudzi uwu ndi moto.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngakhale mutagonjetsa gulu lonse lankhondo la Ababuloni limene likukuthirani nkhondo ndipo mʼmatenti mwawo ndikutsala anthu ovulala okhaokha, amenewo adzabwera ndi kudzatentha mzinda uno.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti ngakhale mukadakantha nkhondo yonse ya Akasidi akumenyana, nanu, ngakhale akadatsala olasidwa okha okha mwa iwo, koma iwowa akadauka yense m'hema wace ndi kutentha mudzi uwu ndi moto.