Jeremiah 37:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamene adafika pa Chipata cha Benjamini, mlonda wina wapamenepo, dzina lake Iriya, mwana wa Selemiya, mwana wa Hananiya, adagwira Yeremiya, nati, “Iwetu ukuthaŵira kwa Ababiloni ati!”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pokhala iye m'chipinda cha Benjamini, kapitao wa alonda anali kumeneko, dzina lake Iriya, mwana wa Selemiya, mwana wa Hananiya; ndipo iye anamgwira Yeremiya mneneri, nati, Ulinkupandukira kwa Ababiloni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma atafika pa Chipata cha Benjamini, mkulu wa alonda amene dzina lake linali Iriya mwana wa Selemiya, mwana wa Hananiya, anagwira mneneri Yeremiyayo ndipo anati, “Iwe ukuthawira kwa Ababuloni!”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pokhala iye m'cipinda ca Benjamini, kapitao wa alonda anali kumeneko, dzina lace Iriya, mwana wa Selemiya, mwana wa Hananiya; ndipo iye anamgwira Yeremiya mneneri, nati, Ulinkupandukira kwa Akasidi.