Jeremiah 37:17 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsiku lina mfumu idatuma anthu kuti akaitane Yeremiya, ndipo idamlandira. Idamufunsa paseri m'nyumba mwake kuti, “Kodi pali mau amene Chauta wakuuza?” Yeremiya adayankha kuti, “Inde, alipo. Inu amfumu mudzaperekedwa m'manja mwa mfumu ya ku Babiloni.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
pamenepo Zedekiya mfumu inatuma, ndi kumtenga iye; ndipo mfumu inamfunsa iye m'tseri m'nyumba mwake, niti, Kodi alipo mau ochokera kwa Yehova? Ndipo Yeremiya, anati, Alipo. Anatinso, Mudzaperekedwa m'dzanja la mfumu ya ku Babiloni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka Mfumu Zedekiya inatuma anthu kuti akayitane Yeremiya ndipo anabwera naye ku nyumba ya mfumu. Atafika mfumu inamufunsa mwamseri kuti, “Kodi pali mawu ena amene Yehova wakuwuza?” Yeremiya anayankha kuti, “Inde. Inu mfumu mudzaperekedwa kwa mfumu ya ku Babuloni.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
pamenepo Zedekiya mfumu inatuma, ndi kumtenga iye; ndipo mfumu inamfunsa iye m'tseri m'nyumba mwace, niti, Kodi alipo mau ocokera kwa Yehova? Ndipo Yeremiya, anati, Alipo, Anatinso, Mudzaperekedwa m'dzanja la mfumu ya ku Babulo.