Jeremiah 37:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo adafunsa mfumu Zedekiya kuti, “Kodi ndakulakwirani chiyani inuyo, aphungu anu, kapena anthu anu kuti mundiponye m'ndende?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yeremiya anati kwa mfumu Zedekiya, Ndachimwira inu chiyani, kapena atumiki anu, kapena anthu awa, kuti mwandiika m'nyumba yandende?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamenepo Yeremiya anafunsa Mfumu Zedekiya kuti, “Kodi ndakulakwirani chiyani inuyo kapena akuluakulu anu kapenanso anthu awa, kuti mundiyike mʼndende?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yeremiya anati kwa mfumu Zedekiya, Ndacimwira inu ciani, kapena atumiki anu, kapena anthu awa, kuti mwandiika m'nyumba yandende?