Jeremiah 37:21 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamenepo mfumu Zedekiya adalamula kuti Yeremiya asungidwe ku bwalo la alonda. Tsono ankamupatsa chakudya tsiku ndi tsiku, mtanda umodzi wa buledi. Ankamugula kwa anthu opanga buledi, mpaka buledi yense mumzindamo adatha. Motero Yeremiya adakhala m'bwalo la alonda.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Zedekiya mfumu analamula, ndipo anamuika Yeremiya m'bwalo la kaidi, tsiku ndi tsiku, nampatsa mkate wofuma kumseu wa oumba mikate, mpaka unatha mkate wonse wa m'mudzi. Ndipo Yeremiya anakhala m'bwalo la kaidi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono Mfumu Zedekiya analamula kuti Yeremiya asungidwe mʼbwalo la alonda. Ankamupatsa buledi tsiku ndi tsiku amene ankamugula kwa ophika buledi. Anapitiriza kutero mpaka buledi yense anatha mu mzindamo. Choncho Yeremiya anapitirira kukhala mʼbwalo la alonda.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Zedekiya mfumu analamula, ndipo anamuika Yeremiya m'bwalo la kaidi, tsiku ndi tsiku, nampatsa mkate wofuma ku mseu wa oumba mikate, mpaka unatha mkate wonse wa m'mudzi. Ndipo Yeremiya anakhala m'bwalo la kaidi.