Jeremiah 37:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono mfumu Zedekiya adatuma Yehukala, mwana wa Semaliya ndi wansembe Zefaniya, mwana wa Maseiya, kwa mneneri Yeremiya kukamuuza kuti, “Mutipempherere kwa Chauta, Mulungu wathu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Zedekiya mfumu anatuma Yehukala mwana wa Selemiya, ndi Zefaniya mwana wa Maaseiya wansembe, kwa Yeremiya mneneri, kukanena, Mutipemphereretu kwa Yehova Mulungu wathu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono Zedekiya anatuma Yehukali mwana wa Selemiya ndi wansembe Zefaniya mwana wa Maseya kwa mneneri Yeremiya ndi uthenga uwu: “Chonde tipempherereni kwa Yehova Mulungu wathu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Zedekiya mfumu anatuma Yehukali mwana wa Selemiya, ndi Zefaniya mwana wa Maseya wansembe, kwa Yeremiya mneneri, kukanena, Mutipemphereretu kwa Yehova Mulungu wathu.