Jeremiah 37:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Ine Chauta, Mulungu wa Israele, ndikunena kuti mfumu ya ku Yuda imene idakutuma kuti udzapemphe nzeru kwa Ine, uiwuze kuti, ‘Gulu lankhondo la Farao limene lidaabwera kuti lidzakuthandize, posachedwa libwerera kwao ku Ejipito, dziko lake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Atero Yehova, Mulungu wa Israele: Muzitero kwa mfumu ya Yuda, imene inakutumani inu kwa Ine kuti mundifunse Ine: Taonani, nkhondo ya Farao, yakutulukira kudzathandiza inu, idzabwerera ku Ejipito ku dziko lao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Uyiwuze mfumu ya Yuda imene inakutuma kuti udzapemphe nzeru kwa ine kuti Ine Yehova, Mulungu wa Israeli ndikuti, gulu lankhondo la Farao limene linatuluka kuti lidzakuthandize lidzabwerera kwawo ku Igupto.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Atero Yehova, Mulungu wa Israyeli: Muzitero kwa mfumu ya Yuda, imene inakutumani inu kwa Ine kuti mundifunse Ine: Taonani, nkhondo ya Farao, yakuturukira kudzathandiza inu, idzabwerera ku Aigupto ku dziko lao.