Jeremiah 37:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zimene akunena Chauta ndi izi, akuti musadzinyenge ndi kumaganiza kuti Ababiloni adzachoka ndi kukusiyani. Pepani sadzachoka ai.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Yehova atero: Musadzinyenge, kuti, Ababiloni adzatichokera ndithu; pakuti sadzachoka.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Yehova akuti: Musadzinyenge, nʼkumaganiza kuti, ‘Ndithu Ababuloni adzatisiya.’ Ndithudi sadzakusiyani!
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Yehova atero: Musadzinyenge, kuti, Akasidi adzaticokera ndithu; pakuti sadzacoka.