Jeremiah 38:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo Ebedemeleki adapita ku nyumba ya mfumu ndi anthuwo, nakatenga nsanza m'chipinda cha zovala. Nsanzazo adazitsitsa ndi zingwe m'chitsime m'mene munali Yeremiya.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Ebedemeleki anatenga anthuwo, nalowa nao m'nyumba ya mfumu ya pansi pa nyumba ya chuma, natenga m'menemo nsalu zakale zotaya ndi zansanza zovunda, nazitsitsira ndi zingwe kwa Yeremiya m'dzenjemo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamenepo Ebedi-Meleki anatenga anthuwo, napita nawo ku nyumba ya mfumu ya pansi pa chipinda chosungiramo chuma. Kumeneko anakatengako sanza ndipo anatsitsira sanzazo ndi chingwe mʼchitsime mʼmene munali Yeremiya.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Ebedi-Meleki anatenga anthuwo, nalowa nao m'nyumba ya mfumu ya pansi pa nyumba ya cuma, natenga m'menemo nsaru zakale zotaya ndi zansanza zobvunda, nazitsitsira ndi zingwe kwa Yeremiya m'dzenjemo.