Jeremiah 38:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsiku lina mfumu Zedekiya adaitana mneneri Yeremiya namlandira pa chipata chachitatu cha ku Nyumba ya Chauta. Adamuuza kuti, “Ndifuna kukufunsa kanthu, usati undibisire ai.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mfumu Zedekiya anatuma, namtenga Yeremiya mneneri nalowa naye m'khomo lachitatu la nyumba ya Yehova; ndipo mfumu inati kwa Yeremiya, Ndidzakufunsa iwe kanthu; usandibisire ine kanthu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsiku lina Mfumu Zedekiya anayitana mneneri Yeremiya ndipo anabwera naye ku chipata chachitatu cha Nyumba ya Yehova. Mfumu inawuza Yeremiya kuti, “Ndikufuna kukufunsa kanthu kena, ndipo usandibisire chilichonse.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mfumu Zedekiya anatuma, natntenga Yeremiya mneneri nalowa naye m'khomo lacitatu la nyumba ya Yehova; ndipo mfumu inati kwa Yeremiya, Ndidzakufunsa iwe kanthu; usandibisire ine kanthu.