Jeremiah 38:17 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yeremiya adauza Zedekiya kuti, “Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele, akunena kuti, ‘Ngati mutuluka kukadzipereka kwa akuluakulu a mfumu ya ku Babiloni, mudzakhala ndi moyo, ndipo mzinda uno sadzautentha. Inuyo pamodzi ndi banja lanu mudzakhala moyo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yeremiya anati kwa Zedekiya, Atero Yehova, Mulungu wa makamu, Mulungu wa Israele: Ngati mudzatulukira kwa akulu a mfumu ya ku Babiloni, mudzakhala ndi moyo, ndipo mudziwu sudzatenthedwa ndi moto; ndipo mudzakhala ndi moyo ndi banja lanu;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamenepo Yeremiya anati kwa Zedekiya, “Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti, ‘Ngati mutuluka kukadzipereka kwa ankhondo a mfumu ya ku Babuloni, mudzakhala ndi moyo ndipo mzinda uno sadzawutentha, inu pamodzi ndi banja lanu mudzakhala ndi moyo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yeremiya anati kwa Zedekiya, Atero Yehova, Mulungu wa makamu, Mulungu wa Israyeli: Ngati mudzaturukira kwa akuru a mfumu ya ku Babulo, mudzakhala ndi moyo, ndipo mudziwu sudzatenthedwa ndi moto; ndipo mudzakhala ndi moyo ndi banja lanu;