Jeremiah 38:18 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma mukangopanda kudzipereka kwa akuluakulu a mfumu ya ku Babiloni, mzindawu udzaperekedwa m'manja mwa Ababiloni, ndipo adzautentha, tsono inu simudzapulumuka m'manja mwao.’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
koma ngati simudzatulukira kwa akulu a mfumu ya ku Babiloni, mudziwu udzaperekedwa m'dzanja la Ababiloni, ndipo udzatenthedwa ndi moto, ndipo simudzapulumuka m'manja mwao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma ngati simutuluka kukadzipereka kwa ankhondo a mfumu ya ku Babuloni, mzinda uno udzaperekedwa kwa Ababuloni ndipo adzawutentha; inuyo simudzapulumuka mʼdzanja mwawo.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
koma ngati simudzaturukira kwa akuru a mfumu ya ku Babulo, mudziwu udzaperekedwa m'dzanja la Akasidi, ndipo udzatenthedwa ndi moto, ndipo simudzapulumuka m'manja mwao.