Jeremiah 38:19 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mfumu Zedekiya adauza Yeremiya kuti, “Ndikuwopa Ayuda amene adathaŵira kale kwa Ababiloni. Ndikuwopa kuti Ababiloni adzandipereka kwa Ayudawo, ndipo iwowo adzandichita zoipa.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mfumu Zedekiya anati kwa Yeremiya, Ine ndiopa Ayuda amene anandipandukira ine kunka kwa Ababiloni, angandipereke ine m'manja mwao, angandiseke.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mfumu Zedekiya inati kwa Yeremiya, “Ine ndikuopa Ayuda amene anathawira kale kwa Ababuloni, pakuti mwina Ababuloniwo adzandipereka kwa Ayudawo ndipo iwowo adzandizunza.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mfumu Zedekiya anati kwa Yeremiya, Ine ndiopa Ayuda amene anandipandukira ine kunka kwa Akasidi, angandipereke ine m'manja mwao, angandiseke.