Jeremiah 38:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta akunena kuti, “Aliyense amene atsalire mu mzinda uno adzafa ndi nkhondo, njala ndiponso mliri. Koma aliyense amene atuluke kukadzipereka kwa Ababiloni adzakhala moyo, adzapulumutsa moyo wake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Yehova atero, Iye wakukhala m'mudziwu adzafa ndi lupanga, ndi njala, ndi chaola; koma iye wakutulukira kunka kwa Ababiloni adzakhala ndi moyo, ndipo adzakhala nao moyo wake ngati chofunkha, nadzakhala ndi moyo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Yehova akuti, ‘Aliyense amene akhale mu mzinda muno adzafa ndi nkhondo njala kapena mliri. Koma aliyense amene atatuluke kukadzipereka kwa Ababuloni adzapulumutsa moyo wake; iyeyo adzakhala ndi moyo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Yehova atero, Iye wakukhala m'mudziwu adzafa ndi lupanga, ndi njala, ndi caola; koma iye wakuturukira kunka kwa Akasidi adzakhala ndi moyo, ndipo adzakhala nao moyo wace ngati cofunkha, nadzakhala ndi moyo.