Jeremiah 38:20 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yeremiya adayankha kuti, “Iyai, sadzakuperekani. Ngati mumvera Chauta pa zonse, ndikukuuzani kuti zinthu zonse zidzakuyenderani bwino, ndipo mudzakhala ndi moyo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Yeremiya anati, Sadzakuperekani. Mveranitu mau a Yehova, amene ndinena ndi inu, chomwecho kudzakomera inu, ndipo moyo wanu udzakhalabe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yeremiya anayankha kuti, “Ngati mumvera Yehova ndi kuchita zimene ndakuwuzani, ndiye kuti zinthu zidzakuyenderani bwino. Inu simudzaphedwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma Yeremiya anati, Sadzakuperekani. Mveranitu mau a Yehova, amene ndinena ndi inu, comweco kudzakomera inu, ndipo moyo wanu udzakhalabe.