Jeremiah 38:22 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
akazi onse otsala m'nyumba ya mfumu ya ku Yuda, adzaperekedwa kwa akuluakulu a mfumu ya ku Babiloni. Popita ku Babiloniko, akazi amenewo azidzaimba kuti, “ ‘Abwenzi ako okhulupirika aja adakunyenga, ndipo adakugonjetsa. Tsopano poti miyendo yako yazama m'matope, abwenzi akowo akusiya.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Taonani, akazi onse otsala m'nyumba ya mfumu ya Yuda adzatulutsidwa kunka kwa akulu a mfumu ya ku Babiloni, ndipo akaziwo adzati, Oyanjana nanu anakunyengani, ndi kukuposani inu, mapazi anu amire m'thope, abwerera m'mbuyo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Akazi onse amene atsala mʼnyumba ya mfumu ya Yuda adzaperekedwa kwa akuluakulu a mfumu ya ku Babuloni. Akazi amenewo adzakuwuzani kuti, “ ‘Abwenzi ako okhulupirika aja anakusokeretsa, ndipo anakugonjetsa. Poti tsopano miyendo yako yazama mʼmatope; abwenzi ako aja akusiya.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Taonani, akazi onse otsala m'nyumba ya mfumu ya Yuda adzaturutsidwa kunka kwa akuru a mfumu ya ku Babulo, ndipo akaziwo adzati, Oyanjana nanu anakunyengani, ndi kukuposani inu, mapazi anu amire m'thope, abwerera m'mbuyo.