Jeremiah 38:25 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Akuluakulu akamva kuti ndakhala ndikulankhula nawe, makamaka abwera kwa iwe kudzanena kuti, ‘Utiwuze zimene wauza amfumu, ndi zimene iwowo akuuza, usatibisire, ndipo sitidzakupha.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma akamva akulu kuti ndalankhula ndi iwe, nakafika kwa iwe, ndi kuti kwa iwe, Utifotokozere ife chomwe wanena kwa mfumu; osatibisira ichi, ndipo sitidzakupha iwe; ndiponso zomwe mfumu inanena kwa iwe;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Akuluakulu akamva kuti ndinayankhula nawe ndipo akabwera kwa iwe nʼkudzakufunsa kuti, ‘Tiwuze zimene unanena kwa mfumu ndi zimene mfumu inanena kwa iwe; usatibisire, ukatero tidzakupha,’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma akamva akuru kuti ndalankhula ndi iwe, nakafika kwa iwe, ndi kuti kwa iwe, Utifotokozere ife comwe wanena kwa mfumu; osatibisira ici, ndipo sitidzakupha iwe; ndiponso zomwe mfumu inanena kwa iwe;