Jeremiah 38:27 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Akuluakulu onse adabweradi kwa Yeremiya kudzamufunsa. Iye adaŵayankha monga momwe mfumu idamuuzira. Motero nkhani zao zidathera pomwepo, chifukwa mau aja anali asanamveke kwa munthu wina aliyense.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo akulu onse anadza kwa Yeremiya, namfunsa; ndipo iye ananena nao monga mwa mau onsewo anamuuza mfumu. Ndipo analeka kunena naye; pakuti sikunamveka mlandu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Akuluakulu onse anabweradi kwa Yeremiya kudzamufunsa. Iye anawayankha monga momwe mfumu inamulamula. Choncho palibe amene ananenanso kanthu, pakuti palibe amene anamva zomwe anakambirana ndi mfumu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo akuru onse anadza kwa Yeremiya, namfunsa; ndipo iye ananena nao monga mwa mau onsewo anamuuza mfumu. Ndipo analeka kunena naye; pakuti sikunamveka mlandu.