Jeremiah 38:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono akuluakulu adauza mfumu kuti, “Munthuyu ayenera kuphedwa. Akutayitsa mtima ankhondo ndi anthu onse otsalira mu mzinda, chifukwa cha zolankhula zakezi. Munthu ameneyu sakuŵafunira zabwino anthu, angofuna kuti aonongedwe basi.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo akulu anati kwa mfumu, Munthu uyu aphedwetu; chifukwa analopetsa manja a anthu a nkhondo otsala m'mudzi uno, ndi manja a anthu onse, pakunena kwa iwo mau otero; pakuti munthu uyu safuna mtendere wa anthu awa, koma nsautso yao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono akuluakuluwo anawuza mfumu kuti, “Munthu uyu ayenera kuphedwa. Iye akutayitsa mtima asilikali pamodzi ndi anthu onse amene atsala mu mzinda muno, chifukwa cha zimene akuwawuza. Munthu ameneyu sakufunira zabwino anthuwa koma chiwonongeko chawo.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo akuru anati kwa mfumu, Munthu uyu aphedwetu; cifukwa analopetsa manja a anthu a nkhondo otsala m'mudzi uno, ndi manja a anthu onse, pakunena kwa iwo mau otero; pakuti munthu uyu safuna mtendere wa anthu awa, koma nsautso yao.