Jeremiah 38:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho iwo aja adatenga Yeremiya, nakamponya m'chitsime chimene adaakumba Malakiya mwana wa mfumu, m'bwalo la alonda a mfumu. Adamtsitsira m'menemo ndi chingwe. M'chitsimemo munalibe madzi, munali matope okhaokha. Ndipo Yeremiya adamira m'matopemo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anatenga Yeremiya, namponya iye m'dzenje la Malikiya mwana wake wa mfumu, limene linali m'bwalo la kaidi; ndipo anamtsitsa Yeremiya ndi zingwe. Koma m'dzenjemo munalibe madzi, koma thope; namira Yeremiya m'thopemo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho iwo anatenga Yeremiya nakamuponya mʼchitsime cha Malikiya, mwana wa mfumu, chimene chinali mʼbwalo la alonda. Iwo anamutsitsira mʼdzenjemo ndi chingwe. Munalibe madzi koma matope okhaokha, ndipo Yeremiya anamira mʼmatopewo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anatenga Yeremiya, namponya iye m'dzenje la Malikiya mwana wace wa mfumu, limene linali m'bwalo la kaidi; ndipo anamtsitsa Yeremiya ndi zingwe, Koma m'dzenjemo munalibe madzi, koma thope; namira Yeremiya m'thopemo.