Jeremiah 38:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Ebedemeleki, Mkusi wina wofulidwa wogwira ntchito ku nyumba ya mfumu, adamva kuti Yeremiya amponya m'chitsime. Nthaŵi imeneyo nkuti mfumu ili ku Chipata cha Benjamini.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pamene Ebedemeleki Mkusi, mdindo, anamva kuti anamuika Yeremiya m'dzenje; mfumu ilikukhala pa chipata cha Benjamini;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Ebedi-Meleki, Mkusi, mmodzi mwa anthu ofulidwa ogwira ntchito mʼnyumba ya mfumu, anamva kuti Yeremiya anamuponya mʼchitsime. Nthawi imeneyo nʼkuti mfumu ili ku chipata cha Benjamini.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pamene Ebedi-Meleki Mkusi, mdindo, anamva kuti anamuika Yeremiya m'dzenje; mfumu irikukhala pa cipata ca Benjamini;