Jeremiah 38:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Mfumu mbuyanga, anthu aŵa amchita zoipa kwambiri mneneri Yeremiya. Amponya m'chitsime, ndipo poti buledi adatha mu mzinda, adzafa ndi njala m'menemo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mbuyanga mfumu, anthu awa anachita zoipa m'zonse anachitira Yeremiya mneneri, amene anamponya m'dzenje; ndipo afuna kufa m'menemo chifukwa cha njala; pakuti mulibe chakudya china m'mudzimu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Mbuye wanga mfumu, zimene anthu awa amuchitira mneneri Yeremiya ndi zoyipa kwambiri. Iwo amuponya mʼchitsime, ndipo adzafa ndi njala chifukwa buledi watha mu mzinda muno.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mbuyanga mfumu, anthu awa anacita zoipa m'zonse anacitira Yeremiya mneneri, amene anamponya m'dzenje; ndipo afuna kufa m'menemo cifukwa ca njala; pakuti mulibe cakudya cina m'mudzimu.