Jeremiah 39:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pa chaka chachisanu ndi chinai cha ufumu wa Zedekiya ku Yuda, mwezi wakhumi, Nebukadinezara, mfumu ya ku Babiloni, adadza ndi gulu lake lonse lankhondo ku Yerusalemu, nazinga mzindawo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chaka chachisanu ndi chinai cha Zedekiya mfumu ya Yuda, mwezi wakhumi, anadza Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni ndi nkhondo yake yonse ku Yerusalemu, ndi kuumangira misasa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mzinda wa Yerusalemu anawulanda motere: Mʼchaka chachisanu ndi chinayi cha Zedekiya mfumu ya Yuda, mwezi wakhumi, Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni anabwera ndi gulu lake lonse kudzathira nkhondo mzinda wa Yerusalemu ndipo anawuzinga mzindawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Caka cacisanu ndi cinai ca Zedekiya mfumu ya Yuda, mwezi wakhumi, anadza Nebukadirezara mfumu ya ku Babulo ndi nkhondo yace yonse, ndi kuumangira misasa.