Jeremiah 39:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nebuzaradani, mtsogoleri wa alonda ankhondoyo, adasiya anthu okhaokha osauka kwambiri, ndi opanda nkanthu komwe m'dziko la Yuda. Ndipo adaŵapatsa minda yamphesa ndi minda inanso.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma aumphawi a anthu, amene analibe kanthu, Nebuzaradani kapitao wa alonda anawasiya m'dziko la Yuda, nawapatsa mipesa ndi minda nthawi yomweyo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Nebuzaradani, mtsogoleri wa alonda ankhondo anasiya mʼdziko la Yuda anthu ena osauka, amene analibe chilichonse; ndipo anawapatsa minda ya mpesa ndi minda inanso.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma aumphawi a anthu, amene analibe kanthu, Nebuzaradani kapitao wa alonda anawasiya m'dziko la Yuda, nawapatsa mipesa ndi minda nthawi yomweyo.