Jeremiah 39:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Motero Nebuzaradani, mtsogoleri wa alonda ankhondo uja, adanyamuka pamodzi ndi Nebusazibani mtsogoleri wamkulu, Neregali-Sarezere mkulu wolamulira gulu lankhondo linanso ndi akuluakulu onse a mfumu ya ku Babiloni.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Nebuzaradani kapitao wa alonda anatumiza, ndi Nebusazibani, mkulu wa adindo Rabi-Sarisi, ndi Neregali-Sarezere mkulu wa alauli, ndi akulu onse a mfumu ya ku Babiloni;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho Nebuzaradani mtsogoleri wa alonda, Nebusazibani mkulu wa nduna, Nerigali-Sarezeri mlangizi wamkulu wa mfumu ndi akuluakulu onse a mfumu ya ku Babuloni
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Nebuzaradani kapitao wa alonda anatumiza, ndi Nebusazibani, mkuru wa adindo Rabi-Sarisi, ndi Nerigalisarezari mkuru wa alauli, ndi akuru onse a mfumu ya ku Babulo;