Jeremiah 39:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iwowo adakatenga Yeremiya ku bwalo la alonda, nakampereka kwa Gedaliya, mwana wa Ahikamu, mdzukulu wa Safani, kuti amumasule ndi kumtumiza kunyumba kwake. Motero Yeremiya adakakhala ndi anthu ake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
iwonso anatumiza, namchotsa Yeremiya m'bwalo la kaidi, nampereka iye kwa Gedaliya mwana wa Ahikamu, mwana wa Safani, kuti anke naye kwao; momwemo iye anakhala ndi anthu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
anatuma anthu nakamutulutsa Yeremiya mʼbwalo la alonda. Anakamupereka kwa Gedaliya mwana wa Ahikamu, mwana wa Safani, kuti amutumize ku nyumba yake. Ndipo Yeremiya anakhala pakati pa abale ake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
iwonso anatumiza, namcotsa Yeremiya m'bwalo la kaidi, nampereka iye kwa Gedaliya mwana wa Ahikamu, mwana wa Safani, kuti anke naye kwao; momwemo iye anakhala ndi anthu.