Jeremiah 39:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Pita ukauze Ebedemeleki Mkusi uja kuti Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele akunena kuti, ‘Zidzachitikadi zimene ndidaanena za mzinda uno, ndipo nzoipa osati zabwino, ai. Zidzachitikadi pa nthaŵi yake, iwe ukupenya.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pita, ukanene kwa Ebedemeleki Mkusi, kuti, Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele: Taona, ndidzafikitsira mudzi uwu mau anga kuusautsa, osauchitira zabwino; ndipo adzachitidwa pamaso pako tsiku lomwelo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Pita ukamuwuze Ebedi-Meleki, Mkusi, kuti, ‘Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti: Zidzachitikadi zimene ndinanena zokhudza mzinda uno; ndipo zidzakhala zoyipa osati zabwino ayi. Zimenezi zidzachitika pa nthawi yake iwe ukuona.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pita, ukanene kwa Ebedi-Meleki Mkusi, kuti, Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli: Taona, ndidzafikitsira mudzi uwu mau anga kuusautsa, osaucitira zabwino; ndipo adzacitidwa pamaso pako tsiku lomwelo.