Jeremiah 39:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamenepo akuluakulu onse a mfumu ya ku Babiloni adaloŵa nakakhala pa chipata chapakati. Anali aŵa: Neregali-Sarezere, Samugiri-Nebo, Sarisekimu mkulu wa nduna, ndi Neregali-Sarezere winanso mkulu wolamulira gulu lankhondo lapatsogolo, pamodzi ndi akuluakulu ena onse a mfumu ya ku Babiloni.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo akulu onse a mfumu ya ku Babiloni analowa, nakhala m'chipata chapakati, Neregali-Sarezere, Samugiri-Nebo, Sarisekimu, mkulu wa adindo, Nerigalisarezara mkulu wa alauli ndi akulu ena onse a mfumu ya ku Babiloni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamenepo akuluakulu onse a mfumu ya ku Babuloni anabwera nakakhala pa Chipata Chapakati. Akuluwo ndi awa: Nerigali-Sarezeri, Samugara Nebo, Sarisekimu mkulu wa nduna, Nerigali-Sarezeri winanso mlangizi wa mfumu ndi akuluakulu onse a mfumu ya ku Babuloni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo akuru onse a mfumu ya ku Babulo analowa, nakhala m'cipata capakati, Nerigalisarezara, Samgari Nebo, Sarisekimu, mkuru wa adindo, Nerigalisarezara mkuru wa alauli ndi akuru ena onse a mfumu ya ku Babulo.