Jeremiah 39:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamene Zedekiya, mfumu ya ku Yuda, adaŵaona, iyeyo pamodzi ndi ankhondo ake adathaŵa mumzindamo usiku, kudzera ku munda wa mfumu, kubzola pa chipata cha pakati pa zipupa ziŵiri. Adathaŵira ku Araba.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo panali pamene Zedekiya mfumu ya Yuda ndi amuna onse a nkhondo anawaona, anathawa natuluka m'mudzi usiku, panjira pa munda wa mfumu, pa chipata cha pakati pa makoma awiri; ndipo iye anatulukira pa njira ya kuchidikha.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Zedekiya mfumu ya Yuda pamodzi ndi ankhondo ake atawaona, anathawa mu mzindawo usiku podzera ku munda wa mfumu, kudutsa chipata cha pakati pa makoma awiri. Anathawira ku Araba.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo panali pamene Zedekiya mfumu ya Yuda ndi amuna onse a nkhondo anawaona, anathawa naturuka m'mudzi usiku, panjira pa munda wa mfumu, pa cipata ca pakati pa makoma awiri; ndipo iye anaturukira pa njira ya kucidikha.