Jeremiah 39:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma gulu lankhondo la Ababiloni lidamlondola ndi kukamgwira Zedekiyayo ku zigwa za ku Yeriko. Mfumuyo ataigwira, adapita nayo kwa Nebukadinezara, mfumu ya ku Babiloni, ku Ribula m'dziko la Hamati. Ndipo adagamula mlandu wake komweko.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma nkhondo ya Ababiloni inawalondola, nimpeza Zedekiya m'zidikha za Yeriko; ndipo atamgwira, anamtengera kwa Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni ku Ribula m'dziko la Hamati, ndipo iye ananena naye mlandu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma gulu la ankhondo la ku Babuloni linalondola ndi kumupeza Zedekiyayo mʼchigwa cha ku Yeriko. Anamugwira napita naye kwa Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni ku Ribula mʼdziko la Hamati kumene anagamula mlandu wake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma nkhondo ya Akasidi inawalondola, nimpeza Zedekiya m'zidikha za Yeriko; ndipo atamgwira, anamtengera kwa Nebukadirezara mfumu ya ku Babulo ku Ribila m'dziko la Hamati, ndipo iye ananena naye mlandu.