Jeremiah 4:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono ndidati, “Ha, Ambuye Chauta, ndithu mudaŵanyenga anthu aŵa pamodzi ndi a mu Yerusalemu! Mudaŵauza kuti, ‘Mudzakhala pa mtendere,’ koma chonsecho lupanga lili pamutu pao.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndinati, Ha, Yehova Mulungu! Ndithu mwanyenga kwambiri anthu awa ndi Yerusalemu, ndi kuti, Mudzalandira mtendere; koma lupanga lafikira pamoyo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo ine ndinati, “Haa, Ambuye Yehova, ndithu munawanyenga anthu awa pamodzi ndi Yerusalemu pamene munanena kuti, ‘Mudzakhala pa mtendere,’ chonsecho lupanga lili pakhosi pathu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndinati, Ha, Yehova Mulungu! ndithu mwanyenga kwambiri anthu awa ndi Yerusalemu, ndi kuti, Mu'dzalandira mtendere; koma lupanga lafikira pamoyo.