Jeremiah 4:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nthaŵiyo ikadzafika, anthu a mu Yerusalemu adzaŵauza kuti, “Mphepo yotentha yochokera ku magomo am'chipululu ikukuntha pa anthu anga, osatitu mphepo yopetera kapena kuyeretsera zinthu ai.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pa nthawi yomweyo adzati kwa anthu awa ndi kwa Yerusalemu, Mphepo yotentha yochokera kumapiri oti see m'chipululu yopita kwa mwana wamkazi wa anthu anga, yosapetera, yosayeretsa;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nthawi imeneyo anthu awa ndi Yerusalemu adzawawuza kuti, “Mphepo yotentha yochokera ku magomo a mʼchipululu ikuwomba pa anthu anga, osati mphepo yopeta kapena yoyeretsa;
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pa nthawi yomweyo adzati kwa anthu awa ndi kwa Yerusalemu, Mphepo yotentha yocokera ku mapiri oti se m'cipululu yopita kwa mwana wamkazi wa anthu anga, yosaungula, yosayeretsa;