Jeremiah 4:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iwe Yerusalemu, chotsa zoipa mumtima mwako kuti upulumuke. Kodi maganizo ako oipa udzakhala nawobe mpaka liti?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Iwe Yerusalemu, utsuke mtima wako kuchotsa zoipa kuti upulumuke. Maganizo ako achabe agona mwako masiku angati?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwe Yerusalemu, tsuka mtima wako kuchotsa zoyipa kuti upulumuke. Kodi maganizo ako oyipawo udzakhala nawo mpaka liti?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Iwe Yerusalemu, utsuke mtima wako kucotsa zoipa kuti upulumuke. Maganizo ako acabe agona mwako masiku angati?