Jeremiah 4:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Akuti, “Muchenjeze mitundu ya anthu kuti mdani akubwera. Mulengeze kwa anthu a mu Yerusalemu kuti ankhondo akubwera kuchokera ku dziko lakutali, akufuula ndi kudzathira nkhondo mizinda ya Yuda.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mukumbutse mitundu ya anthu; taonani, lalikirani Yerusalemu, kuti owazinga ndi nkhondo afumira kudziko lakutali, nainenera midzi ya Yuda mau ao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo akuti, “Fotokozani zimenezi kwa anthu a mitundu ina, lengezani zimenezi mu Yerusalemu kuti, ‘Ankhondo akubwera kuchokera ku dziko lakutali, akufuwula ndi kudzazinga mizinda ya Yuda.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mukumbutse mitundu ya anthu; taonani, lalikirani Yerusalemu, kuti owazinga ndi nkhondo afumira ku dziko lakutari, nainenera midzi ya Yuda mau ao.