Jeremiah 4:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Zimenezi zakugwerani, inu Ayuda, chifukwa cha makhalidwe anu oipa ndi zochita zanu. Chimenechi ndiye chilango chanu, nchoŵaŵa kwambiri, chokalasa mpaka ku mtima.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Njira yako ndi ntchito zako zinakuchitira izi; ichi ndicho choipa chako ndithu; chili chowawa ndithu, chifikira kumtima wako.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Makhalidwe anu ndi zochita zanu zakubweretserani zimenezi. Chimenechi ndiye chilango chanu. Nʼchowawa kwambiri! Nʼcholasa mpaka mu mtima!”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Njira yako ndi nchito zako zinakucitira izi; ici ndico coipa cako ndithu; ciri cowawa ndithu, cifikira ku mtima wako.