Jeremiah 4:19 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mayo, mayo, ati kupweteka ati! Ha, mtima wanga ukuŵaŵa, ukugunda moti thithithi. Sindingathe kukhala chete. Ndikumva kulira kwa lipenga ndi mfuu yankhondo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Matumbo anga, matumbo anga! Ndipoteka pamtima panga penipeni; mtima wanga sukhala pansi m'kati mwanga; sindithai kutonthola; pakuti wamva, moyo wanga, mau a lipenga, mbiri ya nkhondo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mayo, mayo, ndikumva kupweteka! Aa, mtima wanga ukupweteka, ukugunda kuti thi, thi, thi. Sindingathe kukhala chete. Pakuti ndamva kulira kwa lipenga; ndamva mfuwu wankhondo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Matumbo anga, matumbo anga! ndipoteka pamtima panga peni peni; mtima wanga sukhala pansi m'kati mwanga; sindithai kutonthola; pakuti wamva, moyo wanga, mau a lipenga, mbiri ya nkhondo.