Jeremiah 4:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Muzilumbira moona kuti, ‘Pali Chauta wamoyo.’ Muzichita zimenezi mwachilungamo ndi mokhulupirika. Mukatero, anthu a mitundu yonse adzandipempha kuti ndiŵadalitse, ndipo adzanditamanda.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo udzalumbira, Pali Yehova m'zoonadi, m'chiweruziro, ndi m'chilungamo; ndipo mitundu ya anthu idzadzidalitsa mwa Iye, ndipo mwa Iye adzatamandira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Muzilumbira mokhulupirika ndiponso mwa chilungamo kuti, ‘Pali Yehova wamoyo.’ Mukatero anthu a mitundu ina yonse adzandipempha kuti ndiwadalitse ndipo adzanditamanda.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo udzalumbira, Pali Yehova m'zoonadi, m'ciweruziro, ndi m'cilungamo; ndipo mitundu ya anthu idzadzidalitsa mwa Iye, ndipo mwa Iye adzatamandira.